2 Samueli 20:22 - Buku Lopatulika22 Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka mumzindamo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka pamudzipo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Kenaka mkaziyo mwa nzeru zake adapita kwa anthu, naŵasimbira nkhaniyi. Choncho anthuwo adadula mutu wa Sheba, mwana wa Bikiri, namponyera Yowabu. Pamenepo Yowabu adaliza lipenga, ndipo ankhondo ake adachoka kumzindako, aliyense kupita kwao, ndipo Yowabu adabwerera ku Yerusalemu kwa mfumu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu. Onani mutuwo |