2 Samueli 20:21 - Buku Lopatulika21 Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka mumzinda muno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Mlanduwo suli wotere ai, koma munthu wa ku dziko lamapiri la Efuremu, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri, anakweza dzanja lake pa mfumu Davide; mpereke iye yekha ndipo ndidzachoka kumudzi kuno. Ndipo mkaziyo anati kwa Yowabu, Onani tidzakuponyerani mutu wake kutumphitsa linga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Cholinga si chimenechi. Koma munthu wina wa ku dziko la mapiri la Efuremu, dzina lake Sheba, mwana wa Bikiri, adaukira mfumu Davide. Mumpereke yekhayo, ndipo mzindawu ndiwuleka.” Mkazi uja adauza Yowabu kuti, “Tikuponyerani mutu wake pa khoma.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Nkhani simeneyo ayi. Koma munthu wina wa ku dziko lamapiri la Efereimu, dzina lake Seba mwana wa Bikiri, wawukira mfumu Davide. Muperekeni munthuyo ndipo ine ndidzachoka pa mzinda uno.” Mayiyo anati kwa Yowabu, “Mutu wake tikuponyerani pa khoma pano.” Onani mutuwo |