Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:7 - Buku Lopatulika

7 Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Iyeyo adapangana ndi Yowabu, mwana wa Zeruya, ndiponso Abiyatara wansembe. Choncho iwowo adamtsata Adoniya namamthandiza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Adoniya anagwirizana ndi Yowabu mwana wa Zeruya ndiponso Abiatara wansembe, ndipo iwowa anamuthandiza.

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:7
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu anaitana Ahitofele Mgiloni, phungu wa Davide, kumzinda wake ndiwo Gilo, pamene iye analikupereka nsembe. Ndipo chiwembucho chinali cholimba; pakuti anthu anachulukachulukabe kwa Abisalomu.


Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abiyatara ansembewo kodi? Motero chilichonse udzachimva cha m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abiyatara ansembewo.


Ndipo Yowabu anali woyang'anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;


ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe;


Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,


Ndipo mfumu Solomoni anayankha, nati kwa amai wake, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wake wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkulu wanga; inde ukhale wake, ndi wa Abiyatara wansembeyo, ndi wa Yowabu mwana wa Zeruya.


Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.


ndi wotsatana ndi Ahitofele, Yehoyada mwana wa Benaya, ndi Abiyatara; koma kazembe wa nkhondo ya mfumu ndiye Yowabu.


Adzikhazikitsa mafumu a dziko lapansi, nachita upo akulu pamodzi, Kutsutsana naye Yehova, ndi Wodzozedwa wake, ndi kuti,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa