Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 23:20 - Buku Lopatulika

20 Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Benaya mwana wa Yehoyada, wa ku Kabizeele, anali munthu wolimba mtima amene ankachita ntchito zamphamvu. Iyeyo adapha ankhondo aŵiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina chisanu cha mbee chitagwa, adatsikira m'chitsime, naphamo mkango.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 23:20
19 Mawu Ofanana  

Saulo ndi Yonatani anali okoma ndi okondweretsa m'miyoyo yao, ndipo mu imfa yao sanasiyane; anali nalo liwiro loposa chiombankhanga, anali amphamvu koposa mikango.


Ndipo Yowabu anali woyang'anira khamu lonse la Israele; ndi Benaya, mwana wa Yehoyada, anayang'anira Akereti ndi Apeleti;


Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikane ndi atatu oyamba.


ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m'dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.


Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.


Ndipo Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali ansembe ake.


Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomoni mnyamata wanu, sanatiitane.


Pamenepo Zadoki wansembe, ndi Natani mneneri, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Akereti, ndi Apeleti aja anatsika, nakweza Solomoni pa nyuru ya mfumu Davide, nafika naye ku Gihoni.


Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.


Pamenepo mfumu inalamulira Benaya mwana wa Yehoyada, ndipo iye anatuluka namkwera, namwalira iye. Ndipo ufumu unakhazikika m'dzanja la Solomoni.


Ndi Agadi ena anapatukira kwa Davide ku linga la m'chipululu, ngwazi zamphamvu zozerewera nkhondo, zogwira chikopa ndi mkondo; nkhope zao zikunga nkhope za mikango, ndi liwiro lao longa la ngoma mumapiri:


ndi Benaya mwana wa Yehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti; koma ana a Davide ndiwo oyamba ku dzanja la mfumu.


Pamenepo mafumu a Edomu anadabwa; agwidwa nako kunthunthumira amphamvu a ku Mowabu; okhala mu Kanani onse asungunuka mtima.


Ndipo mizinda ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa