Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 23:21 - Buku Lopatulika

21 ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m'dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 ndipo anapha Mwejipito munthu wokongola, Mwejipito anali nao mkondo m'dzanja lake; koma iyeyo anatsikira kwa iye ndi ndodo, nasolola mkondowo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wa iye mwini.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Adaphanso Mwejipito wina, wa maonekedwe okongola. Mwejipitoyo adaali ndi mkondo m'manja, koma Benaya adapita kwa iyeyo ndi ndodo chabe. Adalanda mkondowo ku manja mwa Mwejipito uja, namupha ndi mkondo wake womwewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Ndipo iye anakanthanso Mwigupto wamkulu msinkhu. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 23:21
5 Mawu Ofanana  

Ndipo Benaya, mwana wa Yehoyada, mwana wa ngwazi wa ku Kabizeeli amene anachita zamphamvu; iye anapha anthu awiri a Mowabu akunga mikango, natsikanso iye napha mkango m'mbuna nyengo ya chipale chofewa;


Izi anachita Benaya mwana wa Yehoyada, natenga dzina mwa ngwazi zitatuzo.


Anaphanso Mwejipito munthu wamkulu, msinkhu wake mikono isanu, ndi m'dzanja la Mwejipito munali mkondo ngati mtanda woombera nsalu; ndipo anamtsikira ndi ndodo, nakwatula mkondo m'dzanja la Mwejipito, namupha ndi mkondo wake womwe.


atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.


Potero Davide anathamanga naima pa Mfilistiyo, nagwira lupanga lake, nalisolola m'chimake, namtsiriza nadula nalo mutu wake. Ndipo pakuona Afilisti kuti chiwinda chao chidafa, anathawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa