Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
2 Samueli 2:7 - Buku Lopatulika Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa chake tsono manja anu alimbike, nimuchite chamuna; pakuti Saulo mbuye wanu wafa, ndi a nyumba ya Yuda anandidzoza ndikhale mfumu yao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nchifukwa chake tsono mulimbe mtima, ndipo muchite chamuna. Paja mbuyanu Saulo adamwalira, ndipo anthu a mtundu wa Yuda andidzoza ine kuti ndikhale mfumu yao.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.” |
Zitapita izo, mau a Yehova anadza kwa Abramu m'masomphenya, kuti, Usaope, Abramu, Ine ndine chikopa chako ndi mphotho yako yaikulukulu.
Ulimbike mtima, ndipo tichite chamuna lero chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu; Yehova nachite chomkomera.
Ndipo tsopano Yehova achitire inu chokoma ndi choonadi; inenso ndidzakubwezerani chokoma ichi, popeza munachita chinthuchi.
Koma Abinere, mwana wa Nere, kazembe wa khamu la ankhondo a Saulo anatenga Isiboseti mwana wa Saulo, namuolotsa nanka naye ku Mahanaimu;
Chomwecho akulu onse a Israele anadza kwa mfumu ku Hebroni; ndipo mfumu Davide anapangana nao pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova; ndipo anamdzoza Davide mfumu ya Israele.
Atatero, anatulutsa mwana wa mfumu, namuika korona, nampatsa buku la umboni, namlonga ufumu, namdzoza, naomba m'manja, nati, Mfumu ikhale ndi moyo.
Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma.
ngwazi zonse zinanyamuka ndi kuchezera usiku kuyenda, natenga mtembo wa Saulo, ndi mitembo ya ana ake, pa linga la Beteseani; nafika ku Yabesi-Giliyadi naitentha kumeneko.
Ndipo pamene Aisraele akukhala tsidya lina la chigwa, ndi iwo akukhala tsidya la Yordani, anaona kuti Aisraele alikuthawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake anafa, iwowa anasiya mizinda yao, nathawa; ndipo Afilisti anadza nakhala m'menemo.
Limbikani, ndipo muchite chamuna, Afilisti inu, kuti mungakhale akapolo a Ahebri, monga iwowa anali akapolo anu. Chitani chamuna nimuponyane nao.