Nehemiya 2:18 - Buku Lopatulika18 Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201418 Ndinawauzanso za dzanja la Mulungu wanga londikhalira mokoma, ndiponso za mau anandiuza mfumu. Nati iwo, Tinyamuke, timange. Chotero anandilimbitsira manja mokoma. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa18 Motero ndidaŵasimbira za m'mene Mulungu wanga adandithandizira ndiponso mau amene mfumu idandiwuza. Apo anthuwo adati, “Tiyeni tiyambepo kumanga.” Choncho adalimbitsana mtima kuti akaiyambe ntchito yabwinoyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero18 Ndinawawuza za mmene Yehova Mulungu wanga anandichitira zabwino ndiponso mawu amene mfumu inandiwuza. Tsono anati, “Tiyeni tiyambenso kumanga.” Kotero analimbitsana mtima kuti ayambenso ntchito yabwinoyi. Onani mutuwo |