Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 2:17 - Buku Lopatulika

17 Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m'mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Pamenepo ndinanena nao, Muona choipa m'mene tilimo, kuti Yerusalemu ali bwinja, ndi zipata zake zotentha ndi moto; tiyeni timange linga la Yerusalemu, tisakhalenso chotonzedwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Tsono ndidaŵauza kuti, “Mukuwona mavuto amene tili nawo. Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake azitentha. Tiyeni timange makoma a Yerusalemu, kuti tisamachitenso manyazi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Ndinawawuza kuti, “Inu mukuona mavuto amene tili nawo. Mukuona kuti mzinda wa Yerusalemu wasanduka bwinja ndipo zipata zake zatenthedwa ndi moto. Tsono tiyeni timangenso makoma a Yerusalemu ndipo sitidzachitanso manyazi.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 2:17
23 Mawu Ofanana  

Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga mu Yuda ndi mu Yerusalemu.


Nanena nane iwo, Otsalawo otsala andende uko kudzikoko akulukutika kwakukulu, nanyozedwa; ndi linga la Yerusalemu lapasuka, ndi zipata zake zatenthedwa ndi moto.


Ndipo ndinatuluka usiku pa Chipata cha ku Chigwa, kunka kuchitsime cha chinjoka, ndi ku Chipata cha Kudzala, ndi kuyang'ana malinga a Yerusalemu adapasukawo, ndi zipata zake zothedwa ndi moto.


Koma olamulira sanadziwe uko ndinamuka, kapena chochita ine; sindidauzenso kufikira pamenepo Ayuda, kapena ansembe, kapena aufulu, kapena olamulira, kapena otsala akuchita ntchitoyi.


Ndi Chipata cha ku Kasupe anachikonza Salumu mwana wa Kolihoze mkulu wa dziko la Mizipa anachimanga, nachikomaniza pamwamba pake, naika zitseko zake, zokowera zake, ndi mipiringidzo yake; ndiponso linga la dziwe la Sela pamunda wa mfumu, ndi kufikira kumakwerero otsikira kumzinda wa Davide.


Pamenepo amitundu adzaopa dzina la Yehova, ndi mafumu onse a dziko lapansi ulemerero wanu.


Mutisandutsa chotonza kwa anzathu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.


Mutiika tikhale onyozeka mwa amitundu, ndi kuti anthu atipukusire mitu.


Ndipo anansi athu amene anatonza Inu muwabwezere chotonza chao, kasanu ndi kawiri kumtima kwao, Ambuye.


Takhala chotonza cha anansi athu, ndi choseketsa ndi cholalatitsa iwo akutizinga.


Ndipo ndidzawapatsa akhale choopsetsa choipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale chitonzo ndi nkhani ndi choseketsa, ndi chitemberero, monse m'mene ndidzawapirikitsiramo.


Ambuye wameza nyumba zonse za Yakobo osazichitira chisoni; wagumula malinga a mwana wamkazi wa Yuda mwa ukali wake; wawagwetsera pansi, waipitsa ufumuwo ndi akalonga ake.


Diso langa limvetsa moyo wanga zowawa chifukwa cha ana aakazi onse a m'mzinda mwanga.


Ndidzakuikanso ukhale bwinja ndi chotonza pakati pa amitundu akukuzinga, pamaso pa onse akupitirirapo.


Tsiku lakumanga malinga ako, tsiku lomwelo lembalo lidzachotsedwa kunka kutali.


Ndipo Nahasi Mwamoni ananena nao, Ndidzapangana nanu, ngati mulola kuti maso a ku dzanja lamanja anu onse akolowoledwe; potero ndidzanyazitsa Aisraele onse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa