Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.
2 Samueli 19:5 - Buku Lopatulika Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang'ono; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu ang'ono; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Yowabu adaloŵa m'nyumba ya mfumu nakafika kwa mfumu, nati, “Inu lero mwachititsa manyazi ankhondo anu amene apulumutsa moyo wanu, ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu. |
Ndipo Davide anakwera pa chikweza cha ku Azitona nakwera nalira misozi; ndipo anafunda mutu wake nayenda ndi mapazi osavala; ndi anthu onse amene anali naye anafunda munthu yense mutu wake ndipo anakwera, nalira misozi pokwerapo.
Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.
Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.
Ndipo mfumu inafunda nkhope yake, nilira ndi mau okweza, Mwana wanga Abisalomu, Abisalomu, mwana wanga, mwana.
m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu.
Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake.
Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva mu Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.