Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 9:27 - Buku Lopatulika

27 Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva mu Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Chifukwa chake munawapereka m'dzanja la adani ao akuwasautsa; koma mu nthawi ya kusautsika kwao anafuula kwa Inu, ndipo munamva m'Mwamba, ndi monga mwa nsoni zanu zambiri munawapatsa apulumutsi akuwapulumutsa m'dzanja la adani ao.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Nchifukwa chake Inu mudaŵapereka kwa adani ao amene ankaŵavuta. Pa nthaŵi imene anali m'mavutoyo, ankalira kwa Inu, ndipo Inu munkaŵamvera muli Kumwambako. Chifukwa cha chifundo chanu chachikulu, mudaŵapatsa atsogoleri amene ankaŵapulumutsa kwa adani ao.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Pamene anazunzidwa anafuwulira kwa Inu, ndipo Inu munawamvera muli kumwambako. Ndipo mwa chifundo chanu chachikulu munkawapatsa atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo.”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 9:27
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anapatsa Israele mpulumutsi, natuluka iwo pansi padzanja la Aaramu; nakhala ana a Israele m'mahema mwao monga kale.


Ndipo Yehova sadanene kuti adzafafaniza dzina la Israele pansi pa thambo; koma anawapulumutsa ndi dzanja la Yerobowamu mwana wa Yehowasi.


Ndipo Yehova anakaniza mbumba yonse ya Israele, nawazunza, nawapereka m'dzanja la ofunkha, mpaka anawataya pamaso pake.


koma Yehova Mulungu wanu muzimuopa, nadzakulanditsani Iyeyu m'dzanja la adani anu onse.


Pakuti Iye anawakweretsera mfumu ya Ababiloni, ndiye anawaphera anyamata ao ndi lupanga, m'nyumba ya malo ao opatulika, osachitira chifundo mnyamata kapena namwali, mkulu kapena nkhalamba; Mulungu anawapereka onse m'dzanja lake.


koma Inu mwa nsoni zanu zazikulu simunawasiye m'chipululu; mtambo woti njo sunawachokere usana kuwatsogolera m'njira, ngakhale moto wa tolo usiku kuwaunikira panjira anayenera kuyendamo.


Natikwatula kwa otisautsa; pakuti chifundo chake nchosatha.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.


Ndipo apulumutsi adzakwera paphiri la Ziyoni kuweruza phiri la Esau; ndipo ufumu udzakhala wake wa Yehova.


Ndipo pamene Yehova anawaukitsira oweruza, Yehova anakhala naye woweruzayo, nawapulumutsa m'dzanja la adani ao masiku onse a woweruzayo; pakuti Yehova anagwidwa chisoni pa kubuula kwao chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa