2 Samueli 3:39 - Buku Lopatulika39 Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo ana aamuna awa a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201439 Ndipo ndikali wofooka ine lero, chinkana ndinadzozedwa mfumu; ndipo amuna awa ana a Zeruya andikakalira mtima; Yehova abwezere wochita choipa monga mwa choipa chake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa39 Tsono ine lero ndafooka kwambiri, ngakhale kuti ndine mfumu yodzozedwa. Ndithu anthu ameneŵa, ana aamuna a Zeruya, akundivutitsa kwambiri. Chauta abwezere munthu wochita zoipa molingana ndi kuipa kwake.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero39 Ndipo lero, ngakhale ine ndine mfumu yodzozedwa, ndilibe mphamvu ndipo ana awa a Zeruya ndi amphamvu kwa ine. Yehova abwezere woyipa molingana ndi zoyipa zake!” Onani mutuwo |
Ndipo Yehova adzambwezera mwazi wake pamutu wake wa iye yekha, popeza iye anawakantha anthu awiri olungama ndi okoma oposa iye mwini, nawapha ndi lupanga, atate wanga Davide osadziwa, ndiwo Abinere mwana wa Nere kazembe wa khamu la nkhondo la Israele, ndi Amasa mwana wa Yetere kazembe wa khamu la nkhondo la Yuda.