2 Samueli 19:6 - Buku Lopatulika6 m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 m'mene mukonda awo akudana nanu, ndi kudana nao amene akukondani. Pakuti lero mwalalikira kuti simusamalira konse akalonga ndi anyamata; pakuti lero ndizindikira kuti tikadafa ife tonse, ndipo akadakhala ndi moyo Abisalomu, pamenepo mukadakondwera ndithu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 poti inu mumakonda anthu odana nanu, ndipo mumadana ndi anthu okukondani. Lero ndiye mwatiwonetsa poyera kuti akalonga ndi ankhondo anu mulibe nawo kanthu. Ha, ndikudziŵa kuti Abisalomu adakakhala moyo, tonsefe nkufa, inu mukadakondwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa. Onani mutuwo |
Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.