2 Samueli 19:7 - Buku Lopatulika7 Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Koma nyamukani tsono mutuluke, mukaŵalimbitse mtima ankhondo anu moŵakondweretsa. Ndithu ndikulumbira pali Chauta kuti, ngati simupita, onse akuthaŵani usiku uno. Ndipo zimenezi zidzakuipirani kwambiri kupambana zoipa zonse zimene zidakugweranipo kale, kuyambira muli mwana mpaka tsopano lino.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Tsopano pitani mukawalimbikitse asilikali anu. Ine ndikulumbira mwa Yehova kuti ngati inu simupita palibe munthu amene adzatsale ali ndi inu polowa dzuwa. Ichi chidzakhala choyipa kwambiri kuposa zovuta zonse zimene zinakugwerani kuyambira muli mnyamata mpaka lero.” Onani mutuwo |