Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m'njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi.
2 Samueli 16:12 - Buku Lopatulika Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kapena Yehova adzayang'anira chosayenerachi alikundichitira ine, ndipo Yehova adzandibwezera chabwino m'malo mwa kunditukwana kwa lero. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mwina mwake Chauta adzaona mavuto anga, nadzandibwezera zabwino chifukwa cha kunditukwanaku.’ ” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwina Yehova adzaona mazunzo anga ndipo adzandibwezera zabwino chifukwa cha kutukwanidwa kumene ndikulandira lero.” |
Chomwecho Davide ndi anthu ake anapita m'njira, ndipo Simei analambalala paphiri popenyana naye, namuka natukwana, namponya miyala, nawaza fumbi.
Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.
Mwapenya; pakuti mumayang'anira chivutitso ndi chisoni kuti achipereke m'manja mwanu; waumphawi adzipereka kwa Inu; wamasiye mumakhala mthandizi wake.
Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.
Monga mpheta ilikuzungulira, ndi namzeze alikuuluka, momwemo temberero la pachabe silifikira.
Kodi Mulungu wakantha Yakobo, monga umo anawakanthira akumkanthawo? Kapena kodi iye waphedwa malinga ndi kuphedwa kwa iwo amene anaphedwa ndi iye?
Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Pakuti chisautso chathu chopepuka cha kanthawi chitichitira ife kulemera koposa kwakukulu ndi kosatha kwa ulemerero;
Ndipo Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu; koma Yehova Mulungu wanu anakusandulizirani tembererolo likhale mdalitso, popeza Yehova Mulungu wanu anakukondani.
ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,
Pakutitu iwo anatilanga masiku owerengeka monga kudawakomera; koma Iye atero, kukatipindulitsa, kuti tikalandirane nao pa chiyero chake.
nalonjeza chowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukira ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wake, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pake.