Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wake, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Solomoni. Ndipo Yehova anamkonda iye,
2 Samueli 12:25 - Buku Lopatulika natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 natumiza ndi dzanja la Natani mneneriyo, namutcha dzina lake Wokondedwa ndi Yehova, chifukwa cha Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndipo adatumiza mau kudzera mwa mneneri Natani kuti mwanayo dzina lake likhale Yedidiya, chifukwa Chauta adaamkonda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo chifukwa chakuti Yehova ankamukonda iyeyo, Yehovayo anatumiza mawu kwa mneneri Natani kuti akamutchule Yedidiya. |
Ndipo Davide anasangalatsa Bateseba mkazi wake, nalowa kwa iye, nagona naye; ndipo anabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Solomoni. Ndipo Yehova anamkonda iye,
Pamenepo Natani ananena ndi Bateseba amake wa Solomoni, nati, Kodi sunamve kuti Adoniya mwana wa Hagiti walowa ufumu, ndipo Davide mbuye wathu sadziwa?
Ndipo anauza mfumu, kuti, Wafika Natani mneneriyo. Ndipo iye anafika pamaso pa mfumu, naweramitsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu.
Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.
ndi Azariya mwana wa Natani anayang'anira akapitao, ndipo Zabudi mwana wa Natani anali wansembe ndi nduna yopangira mfumu,
taona, udzabala mwana, ndiye adzakhala munthu wa phee; ndipo ndidzampumulitsira adani ake onse pozungulirapo, pakuti dzina lake lidzakhala Solomoni; ndipo ndidzapatsa Israele mtendere ndi bata masiku ake;
Ndipo ombadwira mu Yerusalemu ndi awa: Simea, ndi Sobabu, ndi Natani, ndi Solomoni, anai a Batisuwa mwana wamkazi wa Amiyele;
Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa.
Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.
ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.
Za Benjamini anati, Wokondedwa wa Yehova adzakhala ndi Iye mokhazikika; am'phimba tsiku lonse, inde akhalitsa pakati pa mapewa ake.