Nehemiya 13:26 - Buku Lopatulika26 Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201426 Nanga Solomoni mfumu ya Israele sanachimwe nazo zinthu izi? Chinkana mwa amitundu ambiri panalibe mfumu ngati iye, ndi Mulungu wake anamkonda, ndi Mulungu wake anamlonga mfumu ya Aisraele onse; koma ngakhale iye, akazi achilendo anamchimwitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa26 Kodi Solomoni mfumu ya Aisraele suja adachimwa chifukwa cha akazi otereŵa? Pakati pa mitundu ya pansi pano panalibe mfumu yofanafana naye. Mulungu ankamkonda ndipo adamuika kuti akhale mfumu ya Aisraele onse. Komabe akazi achilendo adachimwitsa ngakhale iyeyo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero26 Kodi Solomoni mfumu ya Israeli suja anachimwa chifukwa cha ukwati ngati umenewu. Pakati pa mitundu yambiri panalibe mfumu ngati iyi. Iye anakondedwa ndi Mulungu wake, ndipo Mulungu anamuyika kukhala mfumu ya Israeli yense, koma iyeyo anachimwa chifukwa cha akazi achilendo. Onani mutuwo |