Nehemiya 13:25 - Buku Lopatulika25 Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereke ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna, kapena a inu nokha, ana ao aakazi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereka ana anu akazi kwa ana ao amuna, kapena kutengera ana anu amuna, kapena a inu nokha, ana ao akazi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Tsono ndidakangana nawo ndi kuŵatemberera. Ndidamenya ena mwa iwo ndi kuŵazula tsitsi. Ndipo ndidaŵalumbiritsa m'dzina la Mulungu kuti, “Musadzakwatitse ana anu aakazi kwa amuna achilendo, ndipo ana anu aamuna ndi inu nomwe musakwatire akazi achilendo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Tsono ndinakangana nawo ndi kuwatemberera. Ndinamenya ena mwa anthuwo ndi kuzula tsitsi lawo. Ine ndinawalumbiritsa mʼdzina la Mulungu kuti, “Inu musapereke ana anu aakazi kuti akwatiwe ndi ana awo aamuna kapena inuyo ngakhale ana anu aamuna kukwatira ana awo aakazi. Onani mutuwo |