Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 13:27 - Buku Lopatulika

27 Ndipo kodi tidzamvera inu, kuchita choipa ichi chachikulu chonse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi achilendo?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

27 Ndipo kodi tidzamvera inu, kuchita choipa ichi chachikulu chonse, kulakwira Mulungu wathu ndi kudzitengera akazi achilendo?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

27 Monga tsopano tizimva kuti inunso mumachita choipa chachikulu chomwechi cha kuipira Mulungu pomakwatira akazi achilendo?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

27 Kodi tsopano ife tizimva inu kuti mukuchita choyipa chachikulu chimenechi, kupandukira Yehova Mulungu wathu pomakwatira akazi achilendo?”

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 13:27
5 Mawu Ofanana  

Pamenepo Sekaniya mwana wa Yehiyele, mwana wina wa Elamu, anambwezera Ezara mau, nati, Talakwira Mulungu wathu, tadzitengera akazi achilendo a mitundu ya dzikoli; koma tsopano chimtsalira Israele chiyembekezo kunena za chinthu ichi.


kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatirana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka?


ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.


Masiku aja ndinaonanso Ayudawo anadzitengera akazi a Asidodi, Aamoni, ndi Amowabu,


Ndipo ndani adzavomerezana nanu mlandu uwu? Pakuti monga gawo lake la iye wakumuka kunkhondoko, momwemo lidzakhala gawo lake la iye wakukhala ndi akatundu, adzagawana chimodzimodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa