Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 11:16 - Buku Lopatulika

Ndipo Yowabu atayang'anira mzindawo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yowabu atayang'anira mudziwo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho pamene Yowabu ankazinga mzindawo, adaika Uriya pamalo pamene ankaŵadziŵa kuti pali ankhondo amphamvu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu.

Onani mutuwo



2 Samueli 11:16
13 Mawu Ofanana  

Ndi m'kalatamo analemba kuti, Mumuike Uriya pa msongwe wa nkhondo yolimba, ndipo mumlekerere kuti akanthidwe nafe.


Ndipo akumzindawo anatuluka, namenyana ndi Yowabu; ndipo adagwapo anthu ena, ndiwo a anyamata a Davide; ndi Uriya Muhiti anafanso.


Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa.


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Ndiponso udziwa chimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira, inde chimene anawachitira akazembe awiri aja a magulu a nkhondo a Israele, ndiwo Abinere mwana wa Nere, ndi Amasa mwana wa Yetere, amene aja anawapha, nakhetsa mwazi ngati wa nkhondo masiku a mtendere, napaka mwazi wa nkhondo pa lamba lake la m'chuuno mwake, ndi pa nsapato za pa mapazi ake.


Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mzinda, amene anawalera.


Mkulu akamvera chinyengo, atumiki ake onse ali oipa.


Efuremu azunzika, apsinjika pa mlanduwo; pakuti anafuna mwini wake kutsata lamulolo.


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.