2 Mafumu 10:6 - Buku Lopatulika6 Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mzinda, amene anawalera. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Nawalembera kalata kachiwiri, nati, Mukakhala a ine ndi kumvera mau anga, tengani mitu ya amunawo ana a mbuye wanu, ndi kundidzera ku Yezireele mawa dzuwa lino. Koma ana a mfumu ndiwo amuna makumi asanu ndi awiri, anakhala ndi anthu omveka m'mudzi, amene anawalera. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Tsono Yehu adaŵalemberanso kalata yachiŵiri kuti, “Ngati muli pambuyo panga, ndipo ngati muli okonzeka kundimvera, mudule mitu ya ana a mbuyanu, mudze nayo kwa ine ku Yezireele maŵa nthaŵi yonga yomwe ino.” Ndiye kuti zidzukulu za mfumu 70 zija zinkaleredwa ndi akuluakulu amumzinda aja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Ndipo Yehu anawalembera kalata yachiwiri yonena kuti, “Ngati inu muli mbali yanga ndi kuti mudzandimvera, mudule mitu ya ana a mbuye wanu ndipo mubwere nayo kwa ine ku Yezireeli mawa nthawi ngati yomwe ino.” Tsono ana a mfumu onse 70 anali pamodzi ndi akuluakulu a mu mzindamo, amene ankawalera. Onani mutuwo |