2 Samueli 11:16 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. Onani mutuwoBuku Lopatulika16 Ndipo Yowabu atayang'anira mzindawo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201416 Ndipo Yowabu atayang'anira mudziwo, anaika Uriya pomwe anadziwa kuti pali ngwazi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa16 Choncho pamene Yowabu ankazinga mzindawo, adaika Uriya pamalo pamene ankaŵadziŵa kuti pali ankhondo amphamvu. Onani mutuwo |
“Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake.