2 Samueli 11:21 - Buku Lopatulika21 Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201421 Ndani anakantha Abimeleki mwana wa Yerubeseti? Sadamponyera kodi mphero mkazi wa palinga nafa iye ku Tebezi? Munasendera bwanji pafupi potere pa lingalo? Tsono udzanena, Mnyamata wanu Uriya Muhiti, iyenso adafa, Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa21 Kodi Abimeleki mwana wa Gideoni adamupha ndani? Kodi adamupha si mkazi, pomkunkhunizira mwalawamphero kuchokera pa linga, kotero kuti adafera ku Tebezi? Chifukwa chiyani mudakafika pafupi ndi khoma?’ Pamenepo iweyo ukanene kuti, ‘Wankhondo wanu, Uriya Muhiti uja, nayenso adaphedwa.’ ” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero21 Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ” Onani mutuwo |