Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 1:21 - Buku Lopatulika

Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

“Inu mapiri a ku Gilibowa, pa inu pasagwe mame ndi mvula, pa inu pasapezeke minda yobereka dzinthu. Paja kumeneko adani adanyoza chishango cha munthu wamphamvu, chishango cha Saulo, chosapukutidwapo ndi mafuta.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

“Inu mapiri a ku Gilibowa, musakhalenso ndi mame kapena mvula, kapena minda yobereka zopereka za ufa. Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa, chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta.

Onani mutuwo



2 Samueli 1:21
14 Mawu Ofanana  

Afilisti tsono analimbana nkhondo ndi Israele; ndipo amuna a Israele anathawa pamaso pa Afilisti, nagwa ophedwa paphiri la Gilibowa.


Ndipo m'mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa paphiri la Gilibowa.


Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida, apachikapo zikopa zikwi, ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu.


Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta chikopa.


ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isavumbwepo mvula.


Atero Ambuye Yehova, Tsiku lija anatsikira kumanda ndinachititsa maliro, ndinamphimbira nyanja, ndinachepsa mitsinje yake, ndi madzi aakulu analetseka; ndipo ndinamdetsera Lebanoni, ndi mitengo yonse yakuthengo inafota chifukwa cha uwo.


Nsembe yaufa ndi nsembe yothira zalekeka kunyumba ya Yehova; ansembe, atumiki a Yehova, achita maliro.


Kaya, kapena adzabwerera, nadzalekerera, ndi kusiya mdalitso pambuyo pake, ndiwo nsembe yaufa ndi nsembe yothira ya Yehova Mulungu wanu.


Mutemberere Merozi, ati mthenga wa Yehova, mutemberere chitemberere nzika zake; pakuti sanadzathandize Yehova, kumthandiza Yehova pa achamuna.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Ndipo Afilisti anaponyana ndi Aisraele; Aisraele nathawa pamaso pa Afilisti, nagwa olasidwa m'phiri la Gilibowa.


Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa.