Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 10:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo m'mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa paphiri la Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo m'mawa mwake anafika Afilisti kuvula za ophedwa, napeza Saulo ndi ana ake adagwa pa phiri la Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 M'maŵa mwake, Afilisti atabwera kudzafunkha za anthu ophedwawo, adapeza Saulo ataphedwa pamodzi ndi ana ake pa phiri la Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa pa phiri la Gilibowa.

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 10:8
6 Mawu Ofanana  

nati, Uja ndi mwazi, atha kuonongana mafumu aja, anakanthana wina ndi mnzake; ndipo tsopano, tiyeni Amowabu inu, tikafunkhe.


Ndipo pamene amuna onse a Israele okhala m'chigwamo anaona kuti anathawa, ndi kuti Saulo ndi ana ake adafa, anasiya mizinda yao, nathawa; nadza Afilisti, nakhala m'menemo.


Ndipo anamvula natenga mutu wake, ndi zida zake, natumiza ku dziko la Afilisti pozungulirapo, kulalika m'mafano ao ndi mwa anthu.


Ndipo pofika Yehosafati ndi anthu ake kutenga zofunkha zao, anapezako chuma chambiri, ndi mitembo yambiri ndi zipangizo zofunika, nadzifunkhira, osakhoza kuzisenza zonse; nalimkutenga zofunkhazo masiku atatu, popeza zinachuluka.


Ndipo kunali m'mawa mwake, pakubwera Afilisti kuvula akufawo, anapeza Saulo ndi ana ake atatu ali akufa m'phiri la Gilibowa.


Ndipo Afilistiwo anatenga likasa la Mulungu, nafika nalo kunyumba ya Dagoni, naliika pafupi ndi Dagoni.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa