Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 1:21 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Inu mapiri a ku Gilibowa, musakhalenso ndi mame kapena mvula, kapena minda yobereka zopereka za ufa. Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa, chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

21 Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Mapiri inu a Gilibowa, pa inu pasakhale mame kapena mvula, kapena minda yakutengako zopereka. Pakuti kumeneko zikopa za amphamvu zinatayika koipa, chikopa cha Saulo, monga cha wosadzozedwa ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 “Inu mapiri a ku Gilibowa, pa inu pasagwe mame ndi mvula, pa inu pasapezeke minda yobereka dzinthu. Paja kumeneko adani adanyoza chishango cha munthu wamphamvu, chishango cha Saulo, chosapukutidwapo ndi mafuta.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 1:21
14 Mawu Ofanana  

Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa.


Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa pa phiri la Gilibowa.


Khosi lako lili ngati nsanja ya Davide, yomangidwa bwino ndi yosalala; pa nsanja imeneyo pali zishango 1,000, zishango zonsezo za anthu ankhondo.


Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo, akuyala mphasa, akudya komanso kumwa! Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu!”


Ndidzawusandutsa tsala, udzakhala wosatengulira ndi wosalimira ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina. Ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pa mundapo.”


“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma.


Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova. Ansembe akulira, amene amatumikira pamaso pa Yehova.


Akudziwa ndani? Mwina adzasintha maganizo nʼkutimvera chisoni, nʼkutisiyira madalitso, a chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa kwa Yehova Mulungu wanu.


Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’ ‘Tembererani nzika zake mwaukali, chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova, kulimbana ndi adani ake amphamvu.’


Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi:


Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa.


Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa pa phiri la Gilibowa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa