Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.
2 Akorinto 2:11 - Buku Lopatulika kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 kuti asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziwa machenjerero ake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Cholinga chake nkuti Satana asatichenjerere, paja tikudziŵa njira zake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake. |
Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumkhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.
Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa.
Koma tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.
Pamenepo mkazi wake ananena naye, Kodi uumiriranso kukhala wangwiro? Chitira Mulungu mwano, ufe.
Pomwepo Yesu ananena kwa iye, Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzamgwadira, ndipo Iye yekhayekha udzamlambira.
Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,
alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.
Musakanizana, koma ndi kuvomerezana kwanu ndiko, kwa nthawi, kuti mukadzipereke kwa kupemphera, nimukakhalenso pamodzi, kuti Satana angakuyeseni, chifukwa cha kusadziletsa kwanu.
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.
wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,
Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:
Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.
Koma ndinena kwa inu, kwa otsala a ku Tiatira, onse amene alibe chiphunzitso ichi, amene sanazindikire zakuya za Satana, monga anena, Sindikusanjikizani katundu wina.