Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 2:12 - Buku Lopatulika

12 Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma pamene ndinadza ku Troasi kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Khristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Pamene ndidafika ku Troasi kuti ndikalalike Uthenga Wabwino wonena za Khristu, ndidapeza Ambuye atanditsekulira kale pa khomo kuti ndikagwire ntchito kumeneko.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Tsono nditafika ku Trowa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Khristu, nʼkupeza kuti Ambuye anditsekulira khomo,

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 2:12
20 Mawu Ofanana  

Pamene anafika nasonkhanitsa Mpingo anabwerezanso zomwe Mulungu anachita nao, kuti anatsegulira amitundu pa khomo la chikhulupiriro.


Chotero tinachokera ku Troasi m'ngalawa, m'mene tinalunjikitsa ku Samotrase, ndipo m'mawa mwake ku Neapoli;


ndipo pamene anapita pambali pa Misiya, anatsikira ku Troasi.


Ndipo munali nyali zambiri m'chipinda chapamwamba m'mene tinasonkhanamo.


Paulo, kapolo wa Yesu Khristu, mtumwi woitanidwa, wopatulidwa kukanena Uthenga Wabwino wa Mulungu,


Pakuti panditsegukira pa khomo lalikulu ndi lochititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.


Ngati ena ali nao ulamuliro umene pa inu, si ife nanga koposa? Koma sitinachite nao ulamuliro umene; koma timalola zonse, kuti tingachite chochedwetsa kwa Uthenga Wabwino wa Khristu.


Chomwechonso Ambuye analamulira kuti iwo amene alalikira Uthenga Wabwino akhale ndi moyo ndi Uthenga Wabwino.


Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.


Pakuti sitinyanyampiradi tokha, monga ngati sitinafikire kwa inu; pakuti tinadza kufikira inunso, mu Uthenga Wabwino wa Khristu:


Pakutitu ngati iye wakudza alalikira Yesu wina, amene ife sitinalalikire, kapena ngati mulandira mzimu wa mtundu wina, umene simunalandire, kapena Uthenga Wabwino wa mtundu wina umene simunalandire, mulolana naye bwino lomwe.


Kodi ndachimwa podzichepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?


Koma ngatinso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika;


mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.


Ndipo tatuma pamodzi naye mbaleyo, amene kusimba kwake mu Uthenga Wabwino kuli mu Mipingo yonse;


popeza kuti mwa kuyesa kwa utumiki umene alemekeza Mulungu pa kugonja kwa chivomerezo chanu ku Uthenga Wabwino wa Khristu, ndi kwa kuolowa manja kwa chigawano chanu kwa iwo ndi kwa onse;


ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,


ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu mu Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti akhazikitse inu, ndi kutonthoza inu za chikhulupiriro chanu;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa