Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Akorinto 2:13 - Buku Lopatulika

13 ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Masedoniya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Komabe mumtima mwanga munalibe mtendere, chifukwa sindidampeze Tito, mbale wanga. Tsono ndidatsazikana ndi anthu akumeneko nkupita ku Masedoniya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.

Onani mutuwo Koperani




2 Akorinto 2:13
16 Mawu Ofanana  

Nilawira mamawa mfumu, nimuka mofulumira kudzenje la mikango.


Ndipo atalawirana nao, anachoka Iye, nalowa m'phiri kukapemphera.


ndi kulawirana; ndipo tinalowa m'ngalawa, koma iwo anabwera kwao.


Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.


Ndinadandaulira Tito, ndipo ndinatuma mbaleyo naye. Kodi Tito anakuchenjererani kanthu? Sitinayendayende naye Mzimu yemweyo kodi? Sitinatsate mapazi omwewo kodi?


Chifukwa cha ichi tatonthozedwa; ndipo m'chitonthozo chathu tinakondwera koposa ndithu pa chimwemwe cha Tito, kuti mzimu wake unatsitsimutsidwa ndi inu nonse.


Pakuti ngati ndadzitamandira nako kanthu kwa iye chifukwa cha inu, sindinamvetsedwe manyazi; koma monga tinalankhula zonse ndi inu m'choonadi, koteronso kudzitamandira kwathu kumene kwa Tito, kunakhala choonadi.


Koma ayamikike Mulungu, wakupatsa khama lomweli la kwa inu mu mtima wa Tito.


Nanga za Tito, ali woyanjana wanga ndi wochita nane wa kwa inu; nanga abale athu, ali atumwi a Mipingo, ali ulemerero wa Khristu.


Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso.


Pamenepo popita zaka khumi ndi zinai ndinakweranso kunka ku Yerusalemu pamodzi ndi Barnabasi, ndinamtenganso Tito andiperekeze.


Komatu ngakhale Tito, amene anali ndi ine, ndiye Mgriki, sanamkakamize adulidwe;


pakuti Dema wandisiya ine, atakonda dziko lino lapansi, napita ku Tesalonika; Kresike ku Galatiya, Tito ku Dalamatiya.


kwa Tito, mwana wanga weniweni monga mwa chikhulupiriro cha ife tonse: Chisomo ndi mtendere za kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa