Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 1:25 - Buku Lopatulika

25 alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

25 alowe malo a utumiki uwu ndi utumwi, kuchokera komwe Yudasi anapatukira, kuti apite kumalo a iye yekha.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

25 kuti alandire ntchito iyi ya utumwi, m'malo mwa Yudasi uja amene adaisiya ndipo adapita ku malo omuyenera.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

25 kuti atenge ntchito iyi ya utumwi, imene Yudasi anasiya napita kumalo womuyenera.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 1:25
15 Mawu Ofanana  

Ponenedwa mlandu wake atuluke wotsutsika; ndi pemphero lake likhale ngati kuchimwa.


Pomwepo Iye adzanena kwa iwo a kudzanja lamanzere, Chokani kwa Ine otembereredwa inu, kumoto wa nthawi zonse wokolezedwera mdierekezi ndi angelo ake:


Ndipo amenewa adzachoka kunka ku chilango cha nthawi zonse; koma olungama kumoyo wa nthawi zonse.


Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.


Ndipo pambuyo pake pa nthongoyo, Satana analowa mwa iyeyu. Pamenepo Yesu ananena naye, Chimene uchita, chita msanga.


Pamene ndinakhala nao, Ine ndinalikuwasunga iwo m'dzina lanu amene mwandipatsa Ine; ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayike mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko, kuti lembo likwaniridwe.


amene ife tinalandira naye chisomo ndi utumwi, kuti amvere chikhulupiriro anthu a mitundu yonse chifukwa cha dzina lake;


Ngati sindili mtumwi kwa ena, komatu ndili kwa inu; pakuti chizindikiro cha utumwi wanga ndi inu mwa Ambuye.


(pakuti Iye wakuchita mwa Petro kumtuma kwa odulidwa anachitanso mwa ine kundituma kwa amitundu);


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa