Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 5:1 - Buku Lopatulika

Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Afilisti atalanda Bokosi lachipangano lija, adalinyamula kuchoka nalo ku Ebenezeri nakafika nalo ku Asidodi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Afilisti atalanda Bokosi la Mulungu lija, analitenga kuchoka ku Ebenezeri kupita ku Asidodi.

Onani mutuwo



1 Samueli 5:1
12 Mawu Ofanana  

napereka mphamvu yake mu ukapolo, ndi ulemerero wake m'dzanja la msautsi.


Chaka chimene kazembe wa ku Asiriya anafika ku Asidodi, muja Sarigoni mfumu ya Asiriya anamtumiza iye, ndipo iye anamenyana ndi Asidodi, naugonjetsa.


Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero aakulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.


Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.


Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma mu Gaza ndi mu Gati ndi mu Asidodi anatsalamo ena.


kuyambira Sihori wokhala chakuno cha Ejipito mpaka malire a Ekeroni kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asikeloni, a ku Gati, ndi a ku Ekiro, ndi Avimu;


Ndipo mau a Samuele anafikira kwa Aisraele onse. Ndipo Aisraele anatuluka kukaponyana nkhondo ndi Afilisti, namanga zithando zao ku Ebenezeri; Afilistiwo namanga mu Afeki.


Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.


Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.


Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.


Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.