Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 3:9 - Buku Lopatulika

9 Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero aakulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Bukitsani kunyumba zachifumu za Asidodi, ndi kunyumba zachifumu za m'dziko la Ejipito, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akulu m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ulengeze kwa anthu okhala m'malinga a ku Asidodi, ndiponso kwa okhala m'malinga a ku Ejipito, uŵauze kuti akasonkhane ku mapiri a ku Samariya, akaone zachipwirikiti ndi zachifwamba zimene zikuchitika pakati pa anthu ake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto: “Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya; onani chisokonezo pakati pake ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.”

Onani mutuwo Koperani




Amosi 3:9
22 Mawu Ofanana  

Usachinene ku Gati, usachibukitse m'makwalala a Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasekere, kuti ana aakazi a osadulidwawo angafuule mokondwera.


tidzapeza chuma chonse cha mtengo wake, tidzadzaza nyumba zathu ndi zofunkha;


Mkazi wodekha agwiritsa ulemu; aukali nagwiritsa chuma.


Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.


Ndiponso udzalima minda ya mpesa pa mapiri a Samariya; akuoka adzaoka, nadzayesa zipatso zake zosapatulidwa.


Nenani mu Ejipito, lalikirani mu Migidoli, lalikirani mu Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.


Lalikirani mwa amitundu, falikitsani, kwezani mbendera; falikitsani, musabise; munene, Babiloni wagwidwa, Beli wachitidwa manyazi, Merodaki wathyokathyoka, zosema zake zachitidwa manyazi, mafano ake athyokathyoka.


Koma inu, mapiri a Israele, mudzaphukitsa nthambi zanu, ndi kubalira anthu anga Israele zipatso zanu, pakuti ayandikira kufika.


ndipo ndidzawayesa mtundu umodzi m'dzikomo, pa mapiri a Israele; ndipo mfumu imodzi idzakhala mfumu ya iwo onse, sadzakhalanso mitundu iwiri, kapena kugawanikanso maufumu awiri konse ai.


M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo.


ndipo ndidzalikha okhala mu Asidodi, ndi iye wogwira ndodo yachifumu mu Asikeloni; ndipo ndidzabwezera Ekeroni dzanja langa limlange; ndi Afilisti otsala adzatayika, ati Ambuye Yehova.


Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basani, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani nacho, timwe.


Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake.


Tsoka osalabadirawo mu Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira!


Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando wachiwawa;


kuti tigule osauka ndi ndalama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu.


Kodi m'nyumba ya woipa mukali chuma chosalungama, ndi muyeso wochepa umene ayenera kuipidwa nao?


Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa