Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Amosi 3:8 - Buku Lopatulika

8 Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Mkango ukabangula, kodi sachita mantha ndani? Ambuye Chauta akalankhula, kodi ndani sadzalalika?”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Mkango wabangula, ndani amene sachita mantha? Ambuye Yehova wayankhula, ndani amene sanganenere?

Onani mutuwo Koperani




Amosi 3:8
17 Mawu Ofanana  

Kuomba kwanga nanga, ndi za pa dwale langa: chimene ine ndinachimva kwa Yehova wa makamu Mulungu wa Israele, ndanena kwa inu.


Pakuti Yehova atero kwa ine, Monga mkango, ndi mwana wa mkango wobangula pa nyama yake, sudzaopa mau a khamu la abusa oitanidwa kuupirikitsa, ngakhale kudzichepetsa wokha, chifukwa cha phokoso lao; motero Yehova wa makamu adzatsikira kumenyana nkhondo kuphiri la Ziyoni, ndi kuchitunda kwake komwe.


Ndipo ngati nditi, Sindidzamtchula Iye, sindidzanenanso m'dzina lake, pamenepo m'mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m'mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.


Pamenepo Yeremiya ananena kwa akulu onse ndi kwa anthu onse, kuti, Yehova anandituma ine ndinenere nyumba iyi ndi mzinda uwu mau onse amene mwamva.


Tsiku ilo ndidzameretsera nyumba ya Israele nyanga; ndipo ndidzakutsegulira pakamwa pakati pao; motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo anati, Yehova adzadzuma ali mu Ziyoni, nadzamveketsa mau ake ali mu Yerusalemu; podyetsa abusa padzachita chisoni, ndi mutu wa Karimele udzauma.


Koma munamwetsa Anaziri vinyo, ndi kulamulira aneneri ndi kuti, Musamanenera.


Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwake usanagwire kanthu?


pakuti sitingathe ife kuleka kulankhula zimene tinaziona ndi kuzimva.


Pitani, ndipo imirirani, nimulankhule mu Kachisi kwa anthu onse mau a Moyo umene.


Ndipo anayankha Petro ndi atumwi, nati, Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.


Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.


ndipo mmodzi wa akulu ananena ndi ine, Usalire: taona, Mkango wochokera m'fuko la Yuda, Muzu wa Davide, wapambana kuti akhoza kutsegula buku ndi zizindikiro zake zisanu ndi ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa