Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 8:40 - Buku Lopatulika

40 Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Koma Filipo anapezedwa ku Azoto; ndipo popitapita analalikira Uthenga Wabwino m'midzi yonse, kufikira anadza iye ku Kesareya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Tsono Filipo adapezeka kuti ali ku Azoto. Adapita m'dziko monse akulalika Uthenga Wabwino m'mizinda yonse, mpaka adakafika ku Kesareya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Koma Filipo anapezeka kuti ali ku Azoto ndipo anazungulira konse, kulalikira Uthenga Wabwino mʼmizinda yonse mpaka anakafika ku Kaisareya.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 8:40
21 Mawu Ofanana  

Ndi mtundu wa anthu osokonezeka udzakhala mu Asidodi, ndipo ndidzaononga kudzikuza kwa Afilisti.


Ndipo kunali munthu ku Kesareya, dzina lake Kornelio, kenturiyo wa gulu lotchedwa la Italiya,


Ndipo m'mawa mwake analowa mu Kesareya. Koma Kornelio analikudikira iwo, atasonkhanitsa abale ake ndi mabwenzi ake enieni.


Ndipo taonani, pomwepo amuna atatu anaima pa khomo la nyumba m'mene munali ife, anatumidwa kwa ine ochokera ku Kesareya.


Ndipo pamene Herode adamfunafuna, wosampeza, anafunsitsa odikira nalamulira aphedwe. Ndipo anatsika ku Yudeya kunka ku Kesareya, nakhalabe kumeneko.


Ndipo pamene anakocheza pa Kesareya, anakwera naulonjera Mpingo, natsikira ku Antiokeya.


Ndipo anamuka nafenso ena a ophunzira a ku Kesareya, natenganso wina Mnasoni wa ku Kipro, wophunzira wakale, amene adzatichereza.


Ndipo m'mawa mwake tinachoka, ndipo tinafika ku Kesareya, ndipo m'mene tinalowa m'nyumba ya Filipo mlaliki, mmodzi wa asanu ndi awiri aja, tinakhala naye.


Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku;


iwowo, m'mene anafika ku Kesareya, anapereka kalata kwa kazembe, naperekanso Paulo kwa iye.


Pamenepo Fesito m'mene analowa dziko lake, ndipo atapita masiku atatu, anakwera kunka ku Yerusalemu kuchokera ku Kesareya.


Ndipo atapita masiku ena, Agripa mfumuyo, ndi Berenise anafika ku Kesareya, nalankhula Fesito.


Pamenepo Fesito anayankha, kuti Paulo asungike ku Kesareya, ndi kuti iye mwini adzapitako posachedwa.


Ndipo m'mene adatsotsa mwa iwo masiku asanu ndi atatu kapena khumi okha anatsikira ku Kesareya; ndipo m'mawa mwake anakhala pa mpando wachiweruziro, nalamulira kuti atenge Paulo.


Pamenepo iwo, atatha kuchita umboni ndi kulankhula mau a Ambuye, anabwera kunka ku Yerusalemu, nalalikira Uthenga Wabwino kumidzi yambiri ya Asamariya.


Koma m'mene abale anachidziwa, anapita naye ku Kesareya, namtumiza achokeko kunka ku Tariso.


mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;


Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma mu Gaza ndi mu Gati ndi mu Asidodi anatsalamo ena.


Ndipo Afilisti anatenga likasa la Mulungu, nachoka nalo ku Ebenezeri, napita ku Asidodi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa