1 Samueli 4:13 - Buku Lopatulika Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mudzimo, nanena izi, a m'mudzi monse analira. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atafika, adapeza Eli atakhala pa mpando pambali pa mseu akungoyang'ana, poti ankadera nkhaŵa Bokosi lachipangano la Chauta lija. Pamene Mbenjamini uja adaloŵa mumzindamo, nayamba kusimba zimene zidaachitika kunkhondoko, anthu onse amumzinda adalira kwambiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atafika, anapeza Eli atakhala pa mpando wake mʼmbali mwa msewu, akungoyangʼana, pakuti ankadera nkhawa Bokosi la Mulungu. Munthuyo atalowa mu mzindamo ndi kufotokoza zimene zinachitika ku nkhondo, anthu onse a mu mzindamo anayamba kulira. |
Iwe wokhala mu Aroere, ima panjira, nusuzumire umfunse iye amene athawa, ndi mkazi amene apulumuka; nuti, Chachitidwa chiyani?
Akadzamva ichi Akanani ndi okhala m'dziko onse, adzatizinga ndi kuduliratu dzina lathu padziko lapansi; ndipo mudzachitiranji dzina lanu lalikulu?
Chomwecho Hana anauka atadya mu Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.
Ndipo Eli, pakumva kubuma kwa kulira kwao, anati, Alikupokoseranji? Ndipo munthuyo anafulumira, nadza nauza Eli.
Ndipo kunali, pakunena za likasa la Mulungu, iye anagwa chambuyo pa mpando wake pambali pa chipata, ndi khosi lake linathyoka, nafa iye; popeza anali wokalamba ndi wamkulu thupi. Ndipo adaweruza anthu a Israele zaka makumi anai.