Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 1:9 - Buku Lopatulika

9 Chomwecho Hana anauka atadya mu Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Chomwecho Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wake pa mphuthu ya Kachisi wa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsiku lina iwo atatha kudya ku Silo kuja, Hana adaimirira nakapemphera. Nthaŵi imeneyo nkuti Eli, wansembe uja, ali pa mpando pambali pa khomo la Nyumba ya Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 1:9
9 Mawu Ofanana  

mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndilikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu lili m'kati mwa nsalu zotchinga.


Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.


Liu la Yehova liswetsa nyama zazikazi, ndipo lipulula nkhalango; ndipo mu Kachisi mwake zonse zili m'mwemo zimati, Ulemerero.


Koma ine, mwa kuchuluka kwa chifundo chanu ndidzalowa m'nyumba yanu; ndidzagwada kuyang'ana Kachisi wanu woyera ndi kuopa Inu.


pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am'boole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse.


Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;


Ndipo Samuele anagona kufikira m'mawa, natsegula zitseko za nyumba ya Yehova. Ndipo Samuele anaopa kudziwitsa Eli masomphenyawo.


ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.


Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa