Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.
1 Samueli 4:10 - Buku Lopatulika Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Motero Afilisti adamenya nkhondo ndipo Aisraele adagonjetsedwa kotheratu, nathaŵira kwao. Nthaŵiyo kudaphedwa Aisraele okwanira 30,000, ankhondo oyenda pansi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Afilisti anamenya nkhondo, ndipo anagonjetsa Aisraeli. Iwo anathawa aliyense kwawo. Ankhondo a Aisraeli oyenda pansi okwanira 30,000 anaphedwa. |
Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake.
Ndipo anthu a Israele anakanthidwa pamenepo pamaso pa anyamata a Davide, ndipo kunali kuwapha kwakukulu kumeneko tsiku lomwelo, anthu zikwi makumi awiri.
Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pachipata. Ndipo anauza anthu kuti, Onani mfumu ilikukhala pachipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisraele adathawa, munthu yense ku hema wake.
Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.
Ndipo pakuona Aisraele onse kuti mfumu siinawamvere iwo, anthuwo anayankha mfumu, Tili naye chiyani Davide? Inde tilibe cholowa m'mwana wa Yese; tiyeni kwathu Aisraele inu; yang'aniranitu nyumba yako, Davide. Momwemo Aisraele anachoka kunka ku mahema ao.
Ndipo mfuu unafikira khamu lonse la nkhondo polowa dzuwa, ndi kuti, Yense kumzinda kwao, ndi yense ku dziko la kwao.
Ndipo Abiya ndi anthu ake anawakantha makanthidwe aakulu; nagwa, nafa amuna osankhika zikwi mazana asanu a Israele.
Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali mu Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele.
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.
Koma kudzali, mukapanda kumvera mau a Yehova Mulungu wanu, kusamalira kuchita malamulo ake onse ndi malemba ake amene ndikuuzani lero, kuti matemberero awa onse adzakugwerani ndi kukupezani.
Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Taona, ndidzachita mwa Israele choliritsa mwini khutu kwa munthu yense wakuchimva.
Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.