Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 7:12 - Buku Lopatulika

12 Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali mu Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma pitani tsopano kumalo anga amene anali m'Silo, m'mene ndinaikamo dzina langa poyamba paja, ndi kuona chimene ndinachitira chifukwa cha zoipa za anthu anga Israele.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 “Pitani ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziŵika ndi dzina langa. Mukaone zimene ndidachita kumeneko chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 “ ‘Pitani tsopano ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziwika ndi Dzina langa, ndipo mukaone zimene ndinachita kumeneko chifukwa cha kuyipa kwa anthu anga Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 7:12
13 Mawu Ofanana  

pamenepo Ine ndidzalikha Aisraele kuwachotsera m'dziko ndidawapatsali; ndipo nyumba ino ndapatulira dzina langayi ndidzaitaya kosapenyeka; ndipo Israele adzakhala ngati mwambi ndi nkhani pakati pa anthu onse.


pamenepo ndidzayesa nyumba iyi ifanane ndi Silo, ndipo ndidzayesa mzinda uwu chitemberero cha kwa mitundu yonse ya dziko lapansi.


chifukwa chake ndidzaichitira nyumba iyi, imene itchedwa dzina langa, imene mukhulupirirayi, ndipo ndidzachitira malo amene ndinakupatsani inu ndi makolo anu, monga ndinachitira Silo.


Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.


Koma kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha mwa mafuko anu onse kuikapo dzina lake, ndiko ku chokhalamo chake, muzifunako, ndi kufikako;


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.


Ndipo Yoswa anawalotera maere ku Silo pamaso pa Yehova; ndi apo Yoswa anawagawira ana a Israele dziko, monga mwa magawo ao.


Motero anadziikira fano losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.


Ndipo munthuyo akakwera chaka ndi chaka kutuluka m'mzinda mwake kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Yehova wa makamu mu Silo. Ndipo pomwepo panali ana aamuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Finehasi.


Ndipo iye anati, Ulemerero wachoka kwa Israele; chifukwa likasa la Mulungu lalandidwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa