Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.
1 Samueli 30:4 - Buku Lopatulika Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Davide ndi anthu ake adalira mokweza, mpaka mphamvu zolirira zidaŵathera. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero Davide ndi anthu ake analira mofuwula mpaka analibenso mphamvu zolirira. |
Pakupemphera Ezara tsono, ndi kuwulula ndi kulira misozi, ndi kudzigwetsa pansi pakhomo pa nyumba ya Mulungu, udamsonkhanira mwa Israele msonkhano waukulu ndithu wa amuna, ndi akazi, ndi ana; popeza anthu analira kulira kwakukulu.
Ndipo kunali, pamene mthenga wa Yehova ananena mau awa kwa ana onse a Israele, anthuwo anakweza mau ao, nalira misozi.
Ndipo anthu anadza ku Betele, nakhala pansi pomwepo pamaso pa Mulungu mpaka madzulo; nakweza mau ao ndi kulira misozi yambiri.
Tsono mithengayo inafika ku Gibea kwa Saulo, nalankhula mau amenewa m'makutu a anthu; ndipo anthu onse anakweza mau, nalira misozi.
Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumzindako, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo.
Pakufika iye, onani, Eli analikukhala pampando m'mbali mwa njira, alikuyang'anira, popeza mtima wake unanthunthumira chifukwa cha likasa la Mulungu. Pamene munthu uja anafika m'mzindamo, nanena izi, a m'mzinda monse analira.