Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 30:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumzindako, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo pamene Davide ndi anthu ake anafika kumudziko, onani, unatenthedwa ndi moto; ndi akazi ao ndi ana ao aamuna ndi aakazi anatengedwa ukapolo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Davide ndi anthu ake atafika kumzindako adaupeza utapsa, ndipo akazi ao ndi ana anali atatengedwa ukapolo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 30:3
7 Mawu Ofanana  

Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.


pakuti iye amene Ambuye amkonda amlanga, nakwapula mwana aliyense amlandira.


Taona, ndikupatsa ena otuluka m'sunagoge wa Satana akudzinenera okha ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu anama; taona, ndidzawadzetsa alambire pa mapazi ako, nazindikire kuti Ine ndakukonda.


Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ake, munthu yense ndi a pabanja pake, inde Davide ndi akazi ake awiri, Ahinowamu wa ku Yezireele, ndi Abigaile wa ku Karimele, mkazi wa Nabala.


nagwira akazi ndi onse anali m'mwemo, aakulu ndi aang'ono; sanaphe mmodzi, koma anawatenga, namuka.


Ndipo Davide ndi anthu amene anali naye anakweza mau ao, nalira misozi, kufikira analibe mphamvu yakuliranso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa