nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.
Chinthu chimodzi ndinachipempha kwa Yehova, ndidzachilondola ichi, Kuti ndikhalitse m'nyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, kupenya kukongola kwake kwa Yehova ndi kufunsitsa mu Kachisi wake.
Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;