Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 3:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo kunali nthawi yomweyo Eli atagona m'malo mwake (maso ake anayamba chizirezire osatha kupenya bwino);

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Tsiku lina Eli anali gone kumalo kwake. Maso ake adaali atayamba kupenya mwachimbuuzi, kotero kuti sankatha kupenya bwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Tsiku lina Eli, amene maso anali ofowoka ndi kuti sankatha kuona bwino, anagona pa malo ake.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 3:2
8 Mawu Ofanana  

Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.


Koma maso a Israele anali akhungu mu ukalamba wake, ndipo sanathei kuona. Ndipo anadza nao pafupi; ndipo anapsompsona iwo, nawafungatira.


Koma anakana atate wake, nati, Ndidziwa mwananga, ndidziwa; iyenso adzakhala mtundu wa anthu, iyenso adzakula; koma mphwake adzakhala wamkulu ndi iye, ndipo mbeu zake zidzakhala mitundu yambirimbiri.


Natero mkazi wa Yerobowamu, nanyamuka nanka ku Silo, nalowa m'nyumba ya Ahiya. Koma Ahiya sanathe kupenya, popeza maso ake anali tong'o, chifukwa cha ukalamba wake.


Masiku a zaka zathu ndiwo zaka makumi asanu ndi awiri, kapena tikakhala nayo mphamvudi zaka makumi asanu ndi atatu; koma teronso kukula kwao kumati chivuto ndi chopanda pake; pakuti kumapitako msanga ndipo tithawa ife tomwe.


tsikulo omwe asunga nyumba adzanthunthumira, amuna olimba nadzawerama, akupera nadzaleka poperewera, omwe ayang'ana pamazenera nadzadetsedwa;


Ndipo Eli anali wokalamba ndithu; namva zonse ana ake anachitira Aisraele onse, ndi kuti anagona ndi akazi akusonkhana pa khomo la chihema chokomanako.


Koma Eli anali ndi zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zitatu; ndipo maso ake anangokhala tong'o osapenya.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa