Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 25:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo uzipanga choikaponyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo uzipanga choikapo nyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 “Upange choikaponyale cha golide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi thunthu lake zikhale zagolide, ndipo uchisule ndi nyundo. Zikho zake, ndiye kuti nkhunje ndi maluŵa ake, zonsezo zipangidwire kumodzi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 “Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 25:31
28 Mawu Ofanana  

Ndipo m'kati mwa nyumba munali mikungudza yosemasema, ngati zikho ndi maluwa oti gadaa; munali mikungudza yokhayokha simunaoneke mwala ai.


Ndipo m'khosi mwake munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo.


ndi zoikaponyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide;


mwa kulemera kwakenso cha zoikaponyali zagolide, ndi nyali zake zagolide, mwa kulemera kwake cha choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake; ndi cha zoikaponyali zasiliva, siliva woyesedwa kulemera kwake wa choikaponyali chilichonse, ndi nyali zake, monga mwa ntchito ya choikaponyali chilichonse;


nafukizira Yehova nsembe zopsereza m'mawa ndi m'mawa, ndi madzulo onse, ndi zonunkhira za fungo lokoma, nakonza mkate woonekera pa gome lopatulika, ndi choikaponyali chagolide ndi nyali zake, ziyake madzulo onse; pakuti tisunga chilangizo cha Yehova Mulungu wathu, koma inu mwamsiya Iye.


ndi zoikaponyali ndi nyali zake za golide woona, zakuunikira monga mwa chilangizo chake chakuno cha chipinda chamkati;


Ndipo anapanga zoikaponyali khumi zagolide, monga mwa ziweruzo chake; naziika mu Kachisi, zisanu ku dzanja lamanja, ndi zisanu ku dzanja lamanzere.


Ndipo pa choikaponyali chomwe pakhale zikho zinai zopangika ngati katungurume, mitu yake ndi maluwa ake;


Mitu yao ndi mphanda zao zikhale zotuluka m'mwemo; chonsechi chikhale chosulika chimodzi cha golide woona.


ndi gomelo ndi zipangizo zake, ndi choikaponyali choona ndi zipangizo zake, ndi guwa la nsembe lofukizapo;


ndi choikaponyali cha kuunika, ndi zipangizo zake, ndi nyali zake, ndi mafuta a kuunika;


choikaponyali choona, nyali zake, ndizo nyali zimakonzekazi, ndi zipangizo zake zonse, ndi mafuta a kuunikira;


Akonze nyalizo pa choikaponyali choona pamaso pa Yehova nthawi zonse.


Ndipo anati kwa ine, Uona chiyani? Ndipo ndinati, Ndaona, taonani, choikaponyali cha golide yekhayekha, ndi mbale yake pamwamba pake, ndi nyali zake zisanu ndi ziwiri pamenepo; nyalizo zinali ndi misiwe isanu ndi iwiri, ndiyo ya nyalizo zinali pamwamba pake;


Ndipo udikiro wao ndiwo likasa, ndi gome, ndi choikaponyali, ndi maguwa a nsembe, ndi zipangizo za malo opatulika zimene achita nazo, ndi nsalu yotchinga, ndi ntchito zake zonse.


Ndipo achimange ndi chipangizo zake zonse m'chophimba cha zikopa za akatumbu, ndi kuziika pa chonyamulira.


Ndipo atenge nsalu yamadzi, ndi kuphimba choikaponyali younikira, ndi nyali zake, ndi mbano zake, ndi zoolera zake, ndi zotengera zake zonse za mafuta zogwira nazo ntchito yake.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,


Ndipo mapangidwe ake a choikaponyali ndiwo golide wosula; kuyambira tsinde lake kufikira maluwa ake anachisula; monga mwa maonekedwe ake Yehova anaonetsa Mose, momwemo anachipanga choikaponyali.


Pakuti chihema chidakonzeka, choyamba chija, m'menemo munali choikaponyali, ndi gome, ndi mkate woonekera; paja paitanidwa Malo Opatulika.


Ndipo ndinacheuka kuona wonena mau amene adalankhula ndi ine. Ndipo nditacheuka ndinaona zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide;


chinsinsi cha nyenyezi zisanu ndi ziwiri zimene unaziona padzanja langa lamanja, ndi zoikaponyali zisanu ndi ziwiri zagolide: nyenyezi zisanu ndi ziwiri ndizo angelo a Mipingo isanu ndi iwiri; ndipo zoikaponyali zisanu ndi ziwiri ndizo Mipingo isanu ndi iwiri.


Potero kumbukira kumene wagwerako, nulape, nuchite ntchito zoyamba; koma ngati sutero, ndidzadza kwa iwe, ndipo ndidzatunsa choikaponyali chako, kuchichotsa pamalo pake, ngati sulapa.


Ndipo mu mpando wachifumu mudatuluka mphezi ndi mau ndi mabingu. Ndipo panali nyali zisanu ndi ziwiri za moto zoyaka kumpando wachifumu, ndiyo mizimu isanu ndi iwiri ya Mulungu;


ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa