Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Samueli 3:3 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Nthawiyi nʼkuti nyale ya Mulungu isanazimitsidwe. Samueli anali gone mu Nyumba ya Yehova, kumene kunali Bokosi la Chipangano cha Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona mu Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 ndi nyali ya Mulungu isanazime, Samuele nagona m'Kachisi wa Yehova, m'mene munali likasa la Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Samuelenso anali gone m'Nyumba ya Chauta kumene kunali Bokosi lachipangano la Chauta. Nthaŵiyo nkuti nyale ya Mulungu isanazime.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 3:3
10 Mawu Ofanana  

Mmawa uliwonse ndi madzulo aliwonse amapereka nsembe zopsereza ndi kufukiza lubani kwa Yehova. Iwo amayika buledi pa tebulo loyeretsedwa monga mwa mwambo ndipo amayatsa nyale pa zoyikapo nyale zagolide madzulo aliwonse. Ife timachita zofuna za Yehova Mulungu wathu. Koma inu mwamusiya.


Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova, ichi ndi chimene ndidzachifunafuna: kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga, ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova, ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.


Liwu la Yehova limapindapinda mibawa ndi kuyeretsa nkhalango. Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”


Koma Ine, mwa chifundo chanu chachikulu, ndidzalowa mʼNyumba yanu; mwa ulemu ndidzaweramira pansi kuyangʼana ku Nyumba yanu yoyera.


“Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi.


Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa.


Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa