Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake.
1 Samueli 26:8 - Buku Lopatulika Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Abisai adauza Davide kuti, “Mulungu wapereka mdani wanu kwa inu lero. Bwanji tsono mundilole kuti ndimbaye ndi mkondo kamodzinkamodzi ndi kumkhomerera pansi, sindichita kumbaya kaŵiri.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Abisai anawuza Davide kuti, “Lero Mulungu wapereka mdani wanu mʼmanja mwanu. Tsopano ndiloleni ndimukhomere pansi ndi mkondo wangawu kamodzinʼkamodzi. Sindimulasa kawiri.” |
Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake.
Ndipo Yohanani mwana wa Kareya ananena kwa Gedaliya ku Mizipa m'tseri, kuti, Ndimuketu, ndikaphe Ismaele mwana wa Netaniya, anthu osadziwa; chifukwa chanji adzakuphani inu, kuti Ayuda onse amene anakusonkhanira inu amwazike, ndi otsala a Yuda aonongeke?
Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.
Ndipo Yehova anawapatsa mpumulo pozungulira ponse, monga mwa zonse adalumbirira makolo ao; ndipo pamaso pao sipanaime munthu mmodzi wa adani ao onse; Yehova anapereka adani ao onse m'manja mwao.
Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki.
Ndipo Davide anakhala m'chipululu m'ngaka, nakhala m'dziko la mapiri m'chipululu cha Zifi. Ndipo Saulo anamfunafuna masiku onse, koma Mulungu sadampereke m'dzanja lake.
Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.
Ndipo kunali m'tsogolo mwake kuti mtima wa Davide unamtsutsa chifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo.
Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.
Chomwecho Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Saulo anagona tulo m'kati mwa linga la magaleta, ndi mkondo wake wozika kumutu kwake; ndi Abinere ndi anthuwo anagona pomzinga iye.
Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?