Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nahumu 1:9 - Buku Lopatulika

9 Mulingaliranji chotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Mulingaliranji chotsutsana ndi Yehova? Iye adzatha psiti; nsautso siidzauka kawiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Kodi mukukonzekera kumchita Chauta chiwembu chotani? Adzakuwonongani kotheratu. Sadzalira kuŵalipsira kaŵiri adani akewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova adzachiwononga kotheratu; msautso sudzabweranso kachiwiri.

Onani mutuwo Koperani




Nahumu 1:9
17 Mawu Ofanana  

Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.


Pakuti anakupangirani choipa, anapangana chiwembu, osakhoza kuchichita.


Yehova aphwanya upo wa amitundu, asandutsa chabe zolingirira za mitundu ya anthu.


Kulibe nzeru ngakhale luntha ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.


Tsono musakhale amnyozo, kuti nsinga zanu zingalimbe; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, wandimvetsa za chionongeko chotsimikizidwa padziko lonse lapansi.


nuti, Chomwecho adzamira Babiloni, sadzaukanso chifukwa cha choipa chimene ndidzamtengera iye; ndipo adzatopa. Mau a Yeremiya ndi omwewo.


ndi anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndasolola lupanga langa m'chimake, silidzabwereranso.


Atero Yehova Mulungu, Choipa, choipa cha pa chokha, taona chilinkudza.


Chinkana ndawalangiza ndi lulimbitsa manja ao, andilingiririra choipa.


Mwa iwe watuluka wina wolingalira choipa chotsutsana ndi Yehova, ndiye phungu wopanda pake.


ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;


Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.


Tsiku lija ndidzamchitira Eli zonse ndinaneneratu za pa banja lake, kuchiyamba ndi kuchitsiriza.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa