Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 24:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamchitira iye chokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Saulo mobisika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Apo anthu a Davide aja adamuuza kuti, “Tsiku lija ndi lero limene Chauta ankanena, muja adaakuuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wako m'manja mwako, udzamchita zomwe zidzakukomere.’ ” Tsono Davide adanyamuka, nakadulako chidutswa ku mkanjo wa Saulo, iyeyo osadziŵako ai.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’ ” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 24:4
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwera nao mutu wa Isiboseti kwa Davide ku Hebroni, nanena ndi mfumu, Taonani mutu wa Isiboseti mwana wa Saulo, mdani wanu amene anafuna moyo wanu; Yehova anabwezerera chilango mbuye wanga mfumu lero lino kwa Saulo ndi mbeu yake.


Ngati amuna a m'hema mwanga sanati, ndani adzapeza munthu wosakhuta nyama yomgawira Yobu?


Ndifuula nalo liu langa kwa Yehova; ndi mau anga ndipemba kwa Yehova.


Mundichitire chifundo, Mulungu, mundichitire chifundo; pakuti moyo wanga ukhulupirira Inu, ndipo ndithawira kumthunzi wa mapiko anu, kufikira zosakazazo zidzapita.


Koma akapanda kumlalira, koma Mulungu akalola akomane ndi mnzake, ndidzakuikirani pothawirapo iye.


Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.


Ndipo iye ananena naye, Usaopa; chifukwa dzanja la Saulo atate wanga silidzakupeza; iwe udzakhala mfumu ya Israele, ndipo ine ndidzakhala wotsatana nawe, ichinso Saulo atate wanga achidziwa.


Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.


Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.


Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.


Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa