Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 26:7 - Buku Lopatulika

7 Chomwecho Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Saulo anagona tulo m'kati mwa linga la magaleta, ndi mkondo wake wozika kumutu kwake; ndi Abinere ndi anthuwo anagona pomzinga iye.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

7 Chomwecho Davide ndi Abisai anafika kwa anthuwo usiku; ndipo onani, Saulo anagona tulo m'kati mwa linga la magaleta, ndi mkondo wake wozika kumutu kwake; ndi Abinere ndi anthuwo anagona pomzinga iye.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

7 Choncho Davide ndi Abisai adakaloŵa ku zithando zankhondo usiku. Saulo anali gone m'chithando chake, atazika mkondo wake pansi cha kumutu kwake. Abinere ndi ankhondo onse adaagona momzungulira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

7 Choncho Davide ndi Abisai anapita ku misasa ya ankhondowo usiku. Atafika anangopeza Sauli ali gone mu msasa wake mkondo wake atawuzika pansi pafupi ndi mutu wake, Abineri ndi ankhondo onse anali atagona momuzungulira.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 26:7
5 Mawu Ofanana  

Tsopano mwalamulidwa chitani ichi; muwatengere ana anu ndi akazi magaleta a m'dziko la Ejipito; nimubwere naye atate wanu.


Ndipo Davide anauka m'mamawa, nasiyira nkhosa wozisungira, nasenza zija, namuka, monga anamuuza Yese; ndipo iye anafika ku linga la magaleta, napeza khamu lilikutuluka kunka poponyanira nkhondo lilikufuula.


Pamenepo Davide anayankha nati kwa Ahimeleki Muhiti, ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wake wa Yowabu, nati, Adzatsikira nane ndani kumisasako kwa Saulo? Nati Abisai, Nditsika nanu ndine.


Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa