Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Oweruza 1:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Yuda atakwera, Yehova anapereka Akanani ndi Aperizi m'dzanja lao, ndipo anakantha a iwowa anthu zikwi khumi ku Bezeki.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Onsewo adapita, ndipo Chauta adapereka Akananiwo m'manja mwao pamodzi ndi Aperizi omwe. Ndipo adagonjetsa anthu 10,000 ku Bezeki.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Choncho Ayuda ananyamuka, ndipo Yehova anapereka Akanaani ndi Aperezi mʼmanja mwawo. Ndipo anapha anthu 10,000 ku Bezeki.

Onani mutuwo Koperani




Oweruza 1:4
17 Mawu Ofanana  

Ndipo atafika kwa mfumu, mfumu inati kwa iye, Mikaya, kodi tizimuka ku Ramoti Giliyadi kukathira nkhondo, kapena tileke? Nati iye, Kwerani, ndipo mudzachita mwai, popeza Yehova adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Pamenepo mfumu ya Israele inasonkhanitsa aneneri ngati anthu mazana anai, nanena nao, Kodi ndizimuka kukathira nkhondo pa Ramoti Giliyadi, kapena ndileke? Nati iwo, Kweraniko; popeza Ambuye adzaupereka m'dzanja la mfumu.


Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.


Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.


nakawapereka Yehova Mulungu wanu pamaso panu, ndipo mukawakanthe; pamenepo muwaononge konse; musapangana nao pangano, kapena kuwachitira chifundo.


Potero mudziwe lero lino, kuti Yehova Mulungu wanu ndiye amene aoloka pamaso panu ngati moto wonyeketsa; Iye adzawaononga, Iye adzawagwetsa pamaso panu; potero mudzawapirikitsa, ndi kuwaononga msanga, monga Yehova analankhula ndi inu.


Ndipo Yuda ananena ndi Simeoni mkulu wake, Kwera nane ku gawo langa kuti tiwathire nkhondo Akanani; ndipo inenso ndidzamuka nawe ku gawo lako. Namuka naye Simeoni.


Ndipo anapeza Adoni-Bezeki mu Bezeki, namthira nkhondo nakantha Akanani ndi Aperizi.


Potero Yefita anapita kwa ana a Amoni kuwathira nkhondo; ndipo Yehova anawapereka m'dzanja lake;


Ndipo ana a Israele anakhala pakati pa Akanani, Ahiti, ndi Aamori, ndi Aperizi, ndi Ahivi, ndi Ayebusi;


Ndipo anawawerenga ku Bezeki; ndipo ana a Israele anali zikwi mazana atatu, ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi makumi atatu.


Koma akatero kuti, Kwerani kuno kwa ife, tsono tidzakwera; pakuti Yehova wawapereka m'manja mwathu; ndipo ichi chidzatikhalira chizindikiro.


Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa