Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




1 Samueli 26:23 - Buku Lopatulika

Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalola kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Chauta amadalitsa munthu wokhulupirika ndi wochita zabwino. Chauta anakuperekani m'manja mwanga lero, koma sindidaphe munthu wodzozedwa ufumu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Yehova amadalitsa munthu aliyense wolungama ndi wokhulupirika. Yehova anakuperekani lero mʼmanja mwanga, koma ine sindinakhudze wodzozedwa wa Yehova.

Onani mutuwo



1 Samueli 26:23
16 Mawu Ofanana  

Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho.


Chifukwa chake Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwanga pamaso pake.


mverani Inu pamenepo m'mwambamo, ndipo chitani, weruzani akapolo anu, kumtsutsa woipayo, ndi kumbwezera tchimo lake, ndi kulungamitsa wolungamayo kumbwezera monga chilungamo chake.


Mundikumbukire Mulungu wanga mwa ichi, nimusafafanize zokoma zanga ndinazichitira nyumba ya Mulungu wanga, ndi maudikiro ake.


Pakuti ambwezera munthu monga mwa ntchito yake, napezetsa munthu aliyense monga mwa mayendedwe ake.


Chifundonso ndi chanu, Ambuye, Chifukwa Inu mubwezera munthu aliyense monga mwa ntchito yake.


Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe choipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakuchimwirani, chinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire.


Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera chilango kwa inu.


Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.


Pakuti munthu akapeza mdani wake, adzamleka kodi kuti achoke bwino? Chifukwa chake Yehova akubwezere zabwino pa ichi unandichitira ine lero lomwe.


Yehova andiletse ine kusamula dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova; koma utenge mkondowo uli kumutu kwake, ndi chikho cha madzi, ndipo tiyeni, timuke.


Davide nayankha, nati, Tapenyani mkondo wa mfumu! Abwere mnyamata wina kuutenga.


Koma Davide ananena ndi Abisai, Usamuononge, ndani adzasamula dzanja lake pa wodzozedwa wa Yehova, ndi kukhala wosachimwa?