Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 24:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandiphe pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandichitira zabwino; chifukwa sunandipha pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Lero waonetsa ubwino wako pakuti sudandiphe, Chauta atandipereka kwa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Iweyo lero lino wandifotokozera zabwino zimene wandichitira. Yehova anandipereka mʼdzanja lako koma iwe sunandiphe.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 24:18
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Yuda anavomereza nati, Akhale wolungama wopambana ine, chifukwa ine sindinampatse iye Sela mwana wanga wamwamuna. Ndipo iye sanamdziwenso mkaziyo.


Ndipo simunandipereke m'dzanja la mdani; munapondetsa mapazi anga pali malo.


mdani alondole moyo wanga, naupeze; naupondereze pansi moyo wanga, naukhalitse ulemu wanga m'fumbi.


Pakuti udzaunjika makala amoto pamutu pake; ndipo Yehova adzakupatsa mphotho.


Tsono Davide anati, Kodi amuna a ku Keila adzandipereka ine ndi anyamata anga m'dzanja la Saulo? Ndipo Yehova anati, Adzakupereka.


Ndipo anthu anauza Saulo kuti Davide wafika ku Keila. Ndipo Saulo anati, Mulungu wampereka m'dzanja langa; pakuti atsekerezeka, popeza analowa m'mudzi wa zitseko ndi mipiringidzo.


Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.


Pakuti munthu akapeza mdani wake, adzamleka kodi kuti achoke bwino? Chifukwa chake Yehova akubwezere zabwino pa ichi unandichitira ine lero lomwe.


Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.


Ndipo Abisai anati kwa Davide, Lero Mulungu wapereka mdani wanu m'dzanja lanu; ndiloleni ndimpyoze ndi mkondo, kamodzi kokha, sindidzampyoza kawiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa